Exodus 10:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aejipitowo sankathanso kuwonana, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adachoka pakhomo pake masiku atatu onsewo. Koma Aisraele okha ankakhala koŵala ndithu kuja ankakhalaku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m'nyumba zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe amene anatha kuona mnzake kapena kuchoka pa khomo pake kwa masiku atatu. Koma kumalo kumene kumakhala Aisraeli kunali kowala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
sanaonana, sanaukanso munthu pamalo pace, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israyeli kudayera m'nyumba zao.