Exodus 10:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iyai, zoŵeta zathu zidzapita nafe limodzi ndipo sipadzatsala choŵeta nchimodzi chomwe kuno. Tiyenera kukasankha zoŵeta zokapembedzera nazo Chauta, Mulungu wathu. Mpaka tikafike kumeneko, sitingadziŵe zoyenera kuzigwiritsa ntchito popembedza Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ayi, ife tipita ndi ziweto zathu. Palibe chiweto chilichonse chimene chitatsale kuno, popeza tikasankha komweko ziweto zokapembedzera Yehova. Sitingadziwe zimene tikagwiritse ntchito popembedza Yehova mpaka titakafika kumeneko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; cosatsala ciboda cimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.