Exodus 10:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaka yonse idzaphimbidwa ndi dzombelo, ndipo nthakayo sidzaoneka konse. Lidzadya zonse zomwe sizidaonongeke ndi matalala aja. Lidzadya mitengo yako yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero, kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uti wonse wokuphukirani kuthengo;