Exodus 10:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo nyumba zako, nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, zonse zidzakhala zodzaza ndi dzombe lokhalokha, chinthu chimene atate anu kapenanso makolo anu sadachiwone chibadwire chao.’ ” Tsono Mose adapotoloka nachoka kwa Farao kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’ ” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aaigupto onse; sanaciona cotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, naturuka kwa Farao.