Exodus 10:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nduna za Farao zidafunsa Faraoyo kuti, “Kodi munthu ameneyu adzaleka liti kutivuta chotere? Aloleni anthuwo kuti apite, akapembedze Chauta, Mulungu wao. Kodi simukuwona kuti dziko la Ejipito latheratu kuwonongeka tsopano?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nduna za Farao zinamufunsa kuti, “Kodi munthu uyu adzativutitsa mpaka liti? Aloleni anthuwa apite, kuti akapembedze Yehova Mulungu wawo. Kodi simukuona kuti dziko la Igupto lawonongeka?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata ace a Farao ananena naye, Ameneyo amaticitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Aigupto laonongeka?