Exodus 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adayankha kuti, “Tidzapita tonse ndi ana athu, pamodzi ndi nkhalamba zathu zomwe. Tidzapita ndi ana aamuna, ana aakazi, nkhosa zathu ndi mbuzi zomwe. Tidzatenganso ndi ng'ombe zomwe, chifukwa choti tikachita mwambo wachipembedzo wolemekeza Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anayankha kuti, “Ife tidzapita tonse pamodzi; angʼonoangʼono ndi akuluakulu, ana athu aamuna ndi aakazi, ndiponso ziweto zathu ndi ngʼombe chifukwa tikakhala ndi chikondwerero cha kwa Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akuru athu, ndi ana athu amuna ndi akazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tiri nao madyerero a Yehova.