Exodus 11:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tsopano ndimlanga kamodzi kokha Farao, pamodzi ndi Aejipito onse. Pambuyo pa chilango chimenechi, adzakulolani kuti muchoke. Zoonadi, akadzakulolani kuti muchoke, adzachita chokupirikitsani kuno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzalanga Farao pamodzi ndi Aigupto onse ndi mliri umodzi wotsiriza. Zikadzachitika izi iye adzakulolani kuti mutuluke mʼdziko lino. Ndithu pamene azidzakutulutsani adzachita ngati akukuyingitsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala moo umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Aigupto; pambuyo pace adzakulolani mucoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.