Exodus 11:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mose ndi Aroni adachita zozizwitsa zonsezi pamaso pa Farao. Koma Chauta adamuumitsa mtima Faraoyo, ndipo Aisraelewo sadaŵalole kuti achoke m'dziko mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose ndi Aaroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli atuluke mʼdziko lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose ndi Aroni anacita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wace wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.