Exodus 11:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adafeŵetsa Aejipito kuti akomere Aisraele mtima. Chinanso nkuti Mose anali wotchuka kwambiri m'dziko la Ejipito, pamaso pa nduna za Farao ndiponso pamaso pa anthu onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m'dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anachititsa Aigupto kuti akomere mtima Aisraeli. Komanso Mose anali wotchuka kwambiri mʼdziko la Igupto, pamaso pa nduna za Farao ndi anthu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anawapatsa anthu cisomo pamaso pa Aaigupto. Munthuyo Mose ndiyenso wamkuru ndithu m'dziko la Aigupto, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.