Exodus 11:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo mwana aliyense wachisamba adzaphedwa mu Ejipito monse muno. Kuyambira mwana wachisamba wa Farao, amene ali woyenera kuloŵa ufumu, adzaphedwa, mpaka mwana wachisamba wa mdzakazi amene akupera pa mphero. Mwana woyamba kubadwa wa zoŵeta adzafanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mwana aliyense wamwamuna wachisamba adzafa, kuyambira mwana wamwamuna wa Farao amene amakhala pa mpando waufumu, mpaka mwana wamwamuna wachisamba wa mdzakazi wake amene ali naye pa mtondo, komanso ana oyamba a ziweto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ana onse oyamba a m'dziko la Aigupto adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wacifumu wace, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.