Exodus 11:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine kudzandigwadira, zidzati, “Chokani inu pamodzi ndi anthu anu onse!” Tsono pambuyo pake, ndidzachoka.’ ” Mose adachoka kwa Farao kuja mokwiya kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine, kugwada pamaso panga ndi kunena kuti, “Pita iwe ndi anthu ako onse amene akukutsatirawa! Zimenezi zikadzachitika ine ndidzachoka.” Ndipo Mose anachoka kwa Farao atakwiya kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Turukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pace ndidzaturuka. Ndipo anaturuka kwa Farao wakupsa mtima.