Exodus 12:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Magazi amene mudzawaze pa mphuthu za zitseko ndi pamwamba pa zitseko aja adzakhala ngati chizindikiro. Ine ndikadzaona magaziwo ndidzakudutsani, ndipo ndikadzamakantha anthu a Igupto, mliri wosakazawu sudzakukhudzani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwaziwo udzakhala cizindikilo kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Aigupto,