Exodus 12:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu cikumbutso, muzilisunga la madyerero a Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la madyerero, likhale lemba losatha.