Exodus 12:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku loyamba, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, muzidzachita msonkhano wachipembedzo. Musadzagwire ntchito pa masiku amenewo, koma chakudya chokha choti aliyense adye, mudzatha kukonza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika, ndipo winanso uzikhala pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Musamagwire ntchito masiku onsewa, koma ntchito yokonza chakudya yokha kuti aliyense adye. Izi ndi zimene muzichita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasacitike nchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzicita.