Exodus 12:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muzisunga chikondwerero a Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa ndi pa tsiku limeneli ndinatulutsa magulu anu mʼdziko la Igupto. Muzikondwerera tsiku limeneli pa mibado yonse ngati lamulo lamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinaturutsa makamu anu m'dziko la Aigupto; cifukwa cace muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.