Exodus 12:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku asanu ndi aŵiri onsewo, m'nyumba mwanu musadzapezeke chofufumitsira buledi, chifukwa wina aliyense akadzadya chakudya chofufumitsa, adzachotsedwa pa mtundu wa Aisraele, mlendo ngakhale mbadwa yomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzasadzidwa ku msonkhano wa Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yisiti asamapezeka mʼnyumba zanu kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo aliyense amene adya chakudya chimene muli yisiti, munthu ameneyo ayenera kuchotsedwa mʼgulu la Aisraeli, kaya iyeyo ndi mlendo kapena mbadwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cisapezeke cotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti ali yense wakudya kanthu ka cotupitsa, munthuyo adzasadzidwa ku msonkhano wa Israyeli, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.