Exodus 12:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mose adaitana atsogoleri onse a Aisraele, naŵauza kuti, “Pitani kasankhuleni mwanawankhosa woyenera pa banja lililonse, ndipo muphe nyama ya Paskayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, “Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Mose anaitana akuru onse a Israyeli, nanena nao, Pitani, dzitengereni ana a nkhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paskha.