Exodus 12:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutenge nthambi ya kachitsamba ka hisope, muiviike m'magazi amene mwaŵathira m'mbale. Tsono muwaze magaziwo pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo ndi pamwamba pa chitseko. Wina aliyense asatuluke m'nyumba mwake mpaka m'maŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mutengenso nthambi ya chitsamba cha hisope, muchiviyike mʼmagazi amene mwawayika mʼbeseni ndipo muwaze ena mwa magaziwo pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko. Palibe aliyense wa inu amene adzatuluke mʼnyumba yake mpaka mmawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuubviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asaturuke munthu pakhomo pa nyumba yace kufikira m'mawa.