Exodus 12:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzapita m'dziko lonse la Ejipito, ndi kumapha Aejipito. Azidzati akaona magaziwo pamwamba pa chitseko ndi pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, azidzapitirira khomolo ndipo sadzamulola mngelo wake woononga kuti aloŵe m'nyumba mwanu kuti akupheni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aejipito; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woononga alowe m'nyumba zanu kukukanthani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yehova adzadutsa mʼdziko kudzakantha Aigupto, nʼkuona magazi pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko, Iye adzadutsa khomo limenelo ndipo sadzalola woonongayo kuti alowe mʼnyumba zanu kuti akukantheni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aaigupto; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woonongaalowe m'nyumba zanu kukukanthani.