Exodus 12:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo inu muzidzayankha kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Chauta, chifukwa chakuti adapitirira nyumba za Aisraele ku Ejipito; pamene ankapha Aejipito, nyumba zathu adazisiya.’ ” Atamva zimenezi, anthu adaŵerama pansi, napembedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele m'Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukawawuze kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’ ” Kenaka anthu anawerama napembedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mudzati, Ndiko nsembe ya Paskha wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israyeli m'Aigupto, pamene anakantha Aaigupto, napulumutsa nyumba zathu.