Exodus 12:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adapita, ndipo adamvera zimenezo. Adachitadi zonse zimene Chauta adalamula Mose ndi Aroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israyeli anamuka nacita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anacita momwemo.