Exodus 12:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati pa usiku, Chauta adapha ana onse achisamba m'dziko la Ejipito. Adayambira mwana wachisamba wa Farao amene ankayembekezeka kuloŵa ufumu wake, mpaka ana a akaidi a m'nyumba zamdima za m'ndende. Ana onse oyamba kubadwa a nyama adaphedwanso ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Aigupto, kuyambira mwana woyamba wa Earao wakukhala pa mpando wacifumu wace kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; adi ana oyamba onse a zoweta.