Exodus 12:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulengeze kwa khamu lonse la Aisraele kuti pa tsiku lakhumi la mwezi uno, munthu aliyense adzasankhulire banja lake mwanawankhosa mmodzi. Banja lililonse lidzatenge mwanawankhosa mmodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwana wa nkhosa pabanja.