Exodus 12:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Farao ndi nduna zake zonse, pamodzi ndi Aejipito onse, adadzuka pakati pa usiku, ndipo m'dziko lonse la Ejipito munali maliro okhaokha, chifukwa panalibe banja lopanda mwana wakufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse ndi Aejipito onse; ndipo kunali kulira kwakukulu m'Ejipito; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao ndi nduna zake zonse ndiponso Aigupto onse anadzuka pakati pa usiku, ndipo kunali kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, pakuti panalibe nyumba imene munalibe munthu wakufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Farao anauka usiku, iyendi anyamata ace onse, ndi Aaigupto onse; ndipo kunali kulira kwakukulu m'Aigupto; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo.