Exodus 12:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usiku womwewo Farao adaitana Mose ndi Aroni, ndipo adaŵalamula kuti, “Inu pamodzi ndi Aisraele onse, fulumirani, mutuluke. Asiyeni anthu anga, pitani mukapembedze Chauta monga momwe mudanenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israele; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakati pa usiku Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Nyamukani! Asiyeni anthu anga, inu ndi Aisraeli! Pitani, kapembedzeni Yehova monga munapempha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, turukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israyeli; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.