Exodus 12:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaphika mitanda ya buledi wosafufumitsa wa ufa wokandiratu, yomwe adachoka nayo ku Ejipito kuja. Ufa wabuledi wokandiratuwo unali wosathira chofufumitsira chifukwa anali atapirikitsidwa mwadzidzidzi ku Ejipito kuja. Panalibe nthaŵi yophikira chakudya chao cha kamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapanga buledi wopanda yisiti ndi ufa umene anachoka nawo ku Igupto. Ufawo unalibe yisiti chifukwa anachita kuthamangitsidwa ku Igupto ndipo analibe nthawi yokonzera chakudya chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaoca timitanda topanda cotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Aigupto, popeza sadaikamo cotupitsa; pakuti adawapitikitsa ku Aigupto, ndipo sanathe kucedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.