Exodus 12:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Banja likachepa, kuti silingathe kudya nyama yonseyo, mabanja aŵiri oyandikana aphatikizane pamodzi, monga momwe aliri anthu, tsono onsewo adyere limodzi. Mulinganiziretu chiŵerengero cha anthu odya nyamayo, modziŵa m'mene munthu mmodzi angadyere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzace ali pafupi pa nyumba yace atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwao.