Exodus 12:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usiku wonse Chauta adachezera kutulutsa Aisraelewo m'dziko lija la Ejipito. Nchifukwa chake usiku umenewu ndi wopatulikira Chauta pa mibadwo yonse, kuti ukhale usiku womwe Aisraele onse ayenera kuchezera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usiku wonse Yehova anachezera kutulutsa ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake pa tsiku limeneli Aisraeli onse azichezera usiku wonse kulemekeza Mulungu kamba ka mibado yonse ya mʼtsogolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, cifukwa ca kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israyeli ku mibadwo yao.