Exodus 12:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlendo akakhala pakati panu, namafuna kuti achite nao mwambo wa Paska ya Chauta, muziyamba mwaumbala amuna onse am'banjamo. Pambuyo pake angathe kuloŵa ndi kumachita nao mwambowo. Iyeyo muzimuyesa ngati mbadwa yeniyeni ya Israele. Koma wosaumbalidwa asadyeko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati mlendo wokhala pakati panu angafune kuchita nawo mwambo wa chikondwerero cha Paska, cha Yehovachi, amuna onse a mʼnyumba mwake ayenera kuchita mdulidwe. Akatero muzimutenga ngati mbadwa pakati panu. Koma aliyense wosachita mdulidwe asadye Paska.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko.