Exodus 13:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Farao atauma mtima ndithu, natikaniza kuchoka, Chauta adapha mwana wachisamba aliyense wamwamuna m'dziko lonse la Ejipito. Adapha ana a anthu ndi a zoŵeta omwe. Nchifukwa chake nyama yamphongo iliyonse yoyamba kubadwa imaperekedwa nsembe kwa Chauta. Koma ana athu achisamba aamuna, timachita choombola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao atakanitsitsa kuti asatitulutse, Yehova anapha aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira ana a anthu ndi ziweto zomwe. Nʼchifukwa chake ine ndimapereka nsembe kwa Yehova, chachimuna chilichonse choyamba kubadwa ndipo mwana wamwamuna woyamba kubadwa ndimamuwombola.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Aigupto, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; cifukwa cace ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.