Exodus 13:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Farao ataŵalola Aisraele kuti apite, Mulungu sadaŵadzeretse njira yopita kwa Afilisti, ngakhale kuti imeneyi inali njira yachidule. Mulungu adati, “Sindifuna kuti anthu ameneŵa adzasinthe maganizo ao nadzabwereranso ku Ejipito, akadzangokumana ndi nkhondo yolimbana nawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolera njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati. Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kumka ku Aigupto.