Exodus 13:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adanyamula mafupa aja a Yosefe, chifukwa Yosefeyo anali atalumbiritsa Aisraele aja kuti ndithu mafupawo adzanyamule. Paja Yosefe adaanena kuti, “Ndithu, Mulungu adzakuthandizani, koma mudzayenera kunyamula mafupa angaŵa kuchoka nawo kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israele ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawasiya kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose ananyamula mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe anawalumbiritsa ana a Israeli. Iye anawawuza kuti, “Mulungu adzabwera ndithu kudzakuthandizani, ndipo mudzanyamule mafupa anga pochoka ku malo ano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israyeli ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawwya kuno.