Exodus 13:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ana onse achisamba uŵapereke kwa Ine. Pakati pa Aisraele mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kaya ndi wa munthu kaya ndi wa nyama, ndi wanga ameneyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amace mwa ana a Israyeli, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.