Exodus 13:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yamasana Chauta ankaŵatsogolera ndi chipilala chamtambo namaŵalangiza njira. Ndipo nthaŵi yausiku, ankaŵatsogolera ndi chipilala chamoto, kuŵaunikira njira kuti aziyenda masana ndi usiku womwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yamasana Yehova amakhala patsogolo pa anthu kuwatsogolera njira ndi chipilala cha mtambo, ndipo usiku Yehova ankawatsogolera ndi chipilala cha moto, kuwawunikira njira kuti athe kuyenda masana ndi usiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku;