Exodus 13:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adauza anthu kuti, “Muzikumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito, ku dziko laukapolo, chifukwa Chauta adakutulutsani kumeneko ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye chilichonse chofufumitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku linu limene munaturuka m'Aigupto, m'nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakuturutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka cotupitsa.