Exodus 13:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adalonjeza makolo anu kuti adzakupatsani dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Akadzakuloŵetsani m'dziko limenelo, muzidzachita mwambo umenewu mwezi uno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanaani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi, muzikachita mwambo uwu mwezi uno.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.