Exodus 13:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limenelo muzidzauza ana anu kuti, ‘Tikuchita zonsezi chifukwa cha zimene Chauta adatichitira pamene tinkachoka ku Ejipito.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero cifukwa comwe Yehova anandicitira ine poturuka ine m'Aigupto,