Exodus 13:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lamulo limeneli lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa padzanja panu, kapena chikumbutso chomangidwa pamphumi panu. Motero malamulo a Chauta sadzachoka konse pakamwa panu, chifukwa Iye adakutulutsani ku Ejipito ndi dzanja lake lamphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chikumbutso pakati pa maso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cizikhala ndi iwe ngati cizindikilo pa dzanja lako, ndi cikumbutso pakati pa maso ako; kuti cilamulo ca Yehova cikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakuturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.