Exodus 14:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Farao atayandikira, Aisraele aja adaona Aejipito akuŵalondola, ndipo adachita mantha kwambiri, nayamba kulira mofuula kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Farao anayandikira. Ndipo Aisraeli ataona kuti Aigupto akuwatsatira, anachita mantha aakulu ndipo anafuwula kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israyeli anatukula maso ao, taonani, Aaigupto alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israyeli anapfuulira kwa Yehova.