Exodus 14:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ife tisanachoke ku Ejipito, sitidakuuzirenitu zimenezi? Ife tidaanena kuti, ‘Mutileke, tikhalebe akapolo a Aejipito.’ Zidakatikomera ife kukhalabe akapolo kupambana kuti tifere kuchipululu kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Si awa mauwo tinalankhula nanu m'Ejipito ndi kuti, Tilekeni, kuti tigwirire ntchito Aejipito? Pakuti kutumikira Aejipito kutikomera si kufa m'chipululu ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, ‘Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Si awa maowo tinalankhula nanu m'Aigupto ndi kuti, Tliekeni, kuti tigwirire nchito Aaigupto? pakuti kutumikira Aaigupto kutikomera si kufa m'cipululu ai.