Exodus 14:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mose adayankha anthuwo kuti, “Musaope! Limbikani, ndipo muzingopenya zimene Chauta achite lero lino pofuna kukupulumutsani. Aejipito amene mukuŵaona lerowo, simudzaŵaonanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, cirimikani, ndipo penyani cipulumutso ca Yehova, cimene adzakucitirani lero; pakuti Aaigupto mwawaona lerowa simudzawaonansokonse.