Exodus 14:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo pompo Chauta adaumitsa nyanja ija, pogwiritsa ntchito mphepo yamkuntho yakuvuma, imene idaomba usiku wonse ndi kuumitsa nyanjayo. Madziwo adagaŵikana,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mose anatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo Yehova pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kummawa imene inawomba usiku wonse anabweza madzi ndi kuwumitsa nyanja ija. Choncho nyanja ija inagawanika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.