Exodus 14:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mose adatambalitsa dzanja lake ku nyanja, ndipo m'mene kunkacha, nkuti madziwo akubwerera m'malo mwake. Aejipitowo adayesa kuthaŵa, koma Chauta adaŵabweza momwe m'nyanjamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ake mbandakucha; ndipo Aejipito pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aejipito m'kati mwa nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ace mbanda kuca; ndipo Aaigupto pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aaigupto m'kati mwa nyanja.