Exodus 14:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzamuumitsa mtima Farao, ndipo adzalondola Aisraelewo. Tsono ndikadzagonjetsa Farao pamodzi ndi gulu lonse lankhondo, ndidzalandira ulemu, ndipo Aejipito onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Choncho Aisraele adachita zonse monga momwe adaŵauzira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalimbitsa mtima wace wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yace yonse; pamenepo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, Ndipo anacita comweco.