Exodus 14:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva kuti anthu athaŵa, Farao, mfumu ya ku Ejipito, pamodzi ndi nduna zake zonse, adasintha maganizo pa za Aisraelewo. Adati, “Kodi ife tachitapo chiyani pamenepa? Talola Aisraele kuti athaŵe ndi kuleka kutitumikira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao, mfumu ya Igupto atamva kuti anthu aja athawa, iye pamodzi ndi nduna zake anasintha maganizo awo pa Israeli ndipo anati, “Ife tachita chiyani? Tawalola Aisraeli kuti apite ndi kuleka kutitumikira?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauza mfumu ya Aigupto kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ace inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ici nciani tacita, kuti talola Israyeli amuke osatigwiriranso nchito?