Exodus 14:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenga magaleta amphamvu 600 pamodzi ndi magaleta ena onse ndipo adaika atsogoleri pa magaleta onsewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a m'Ejipito, ndi akapitao ao onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napita nao magareta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magareta onse a m'Aigupto, ndi akapitao ao onse.