Exodus 14:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaumitsa mtima Farao mfumu ya ku Ejipito, ndipo iye adalondola Aisraele, pamene Aisraele ankachoka monyada.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aigupto, ndipo iye analondola ana a Israyeli; koma ana a Israyeli adaturuka ndi dzanja lokwezeka.