Exodus 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aejipitowo, ndiye kuti akavalo ndi magaleta a Farao, oyendetsa magaletawo, okwera pa akavalo ndi gulu lankhondo la Farao, adalondola Aisraele aja nakaŵapeza pamalo pomwe adaamanga zithando paja, pafupi ndi Pihahiroti, moyang'anana ndi Baala-Zefoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aaigupto anawalondola, ndiwo akavalo ndi magareta onse a Farao, ndi apakavalo ace, ndi nkhondo yace, nawapeza ali kucigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.