Exodus 15:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati, “Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wakwezeka mʼchigonjetso. Kavalo ndi wokwera wake, Iye wawaponya mʼnyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyimbo yolemekeza Mulungu, Pamenepo Mose ndi ana a Israyeli anayimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzayimbira Yehova pakuti wapambanatu; Kavalo ndi wokwera wace anawaponya m'nyanja.