Exodus 15:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onsewo agwidwa ndi mantha oopsa. Iwo akhala chete ngati mwala, chifukwa cha kuwopa mphamvu zanu zazikulu. Angokhala chete mpaka anthu anu, Inu Chauta, atabzola, anthu amene mudaŵaombola mu ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; pa dzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse agwidwa ndi mantha woopsa. Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu, iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu, Inu Yehova atadutsa; inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuopa kwakukuru ndi mantha ziwagwera; Pa dzanja lanu lalikuru akhala cete ngati mwala; Kufikira apita anthu anu, Yehova, Kufikira apita anthu amene mudawaombola.